20/08/2026
Ngati muli mu ndondomeko ya penshoni yomwe imafuna kuti okulembani ntchito ndi inuyo kusonkha ndalama za penshoni yanu (Contributory), zimutanthauza kuti ndalama zanu zopuma pantchito zimasonkhanitsidwa mogwirizana pakati pa inu ndi okulembani ntchito.
Mwachitsanzo, ngati malipiro anu onse (asanachotsedwe misonkho ndi zina) ndi MWK 1,200,000, inuyo mumapereka 5% (MWK 60,000) pamene okulembani ntchito amawonjezera 10% (MWK 120,000). Pamodzi, ndalama zokwana MWK 180,000 zimatumizidwa ku akaunti yanu ya penshoni mwezi uliwonse, zomwe zimapanga MWK 2,160,000 pachaka.
Koma woyang'anira penshoni samangosunga ndalamazo; amaziika mu bizinesi kapena ndalama zopindulitsa (investments) kuti zichuluke. Ngati phindu la ndalama zomwe zayikidwazo mu chaka cha 2025 linali 127%, ndalama zanu zokwana MWK 2,160,000 zimachuluka kufika pa MWK 4,467,256.
Izi zikusonyeza kuti penshoni si nkhani yokhayo yosunga ndalama zomwe inuyo ndi okulembani ntchito, koma ndi njira yowonjezera ndalamazo kudzera mu phindu lomwe limapezeka poika ndalamazo mu investment.
Pakapita nthawi, kupitiriza kupereka ndalama komanso kukula kwa ndalamazo chifukwa cha phindu lopitilira, kumapanga ndalama zambiri, zomwe zimakupatsani chitetezo cha zachuma komanso ulemu pamene mwapuma pantchito.