16/08/2026
MUTU WA KUKAMBIRANA KWATHU:
Palibe Maphunziro, Palibe Kuvota. Palibe Digiri, Palibe Utsogoleri.
Umphawi + kusaphunzira = mavoti kugulitsidwa ndi MK2,000, Ma t-shirt, Mahewu, Chitenje. Etc
Zotsatira zake: Zaka 5 za atsogoleri akudzikondera okha, osati dziko.
LINGALIRO
1. Ovota: Satifiketi ya Sekondale Yapamwamba (MSCE).
Izi zidzathandiza kuti nzika yovota idzikhala yokhayo imene ndi ndiyozindikira bwino chimene ikupanga komanso zidzalimbikitsa ana kusukulu kuchita bwino kuti adzikavota nawo pachitsankho cha dziko m’malo momangolandira zaulere. Izi zidzachepetsanso ndalama zimene zimawonongeka po tsindikiza zovotera za nkhaninkhani za anthu oti sakudziwa kufunika kwa mavoti awo.
2. Otsogolera: Digiri Yochepa ya Yunivesite.
Tiyenera kufuna luso mwa anthu omwe amatitsogolera osati ma MP ngakhalenso President ongofuna kudzilemeletsa okha koma kulephera kulankhula ku Nyumba ya Malamulo.
FUNSO:
Kodi izi ndi za anthu ochepa ophunzira okha?
Kapena ndi kusintha komwe Malawi ikufunikira kuti tithetse ndale za zopatsa?
Perekani maganizo anu pansipa 👇